Back to News
January 23, 2026
news
MP Maureen Namwali walonjeza zokwanilitsa zitukuko zonse zomwe adalonjeza.
Phungu wa dera la Thyolo-Goliati Maureen Namwali wati mkumano omwe udalipo ndi adindo osiyanasiyana msabatayi ofuna kuunika zitukuko zomwe zikuyembekezeka kuchitika mundondomeko ya chuma ya 2026/2027 Udali ofunika chifukwa wapereka mphamvu ku wanthu pa zitukuko zomwe zikufunika ku dera la Thyolo-Goliati.
Olemekezeka a Namwali munthawi yokopa anthu adalonjeza zokumva maganizo a mzika pachitukuko chomwe chikufunikira kudera kuti chikhale chopundulira anthu akuderalo komaso kutha kuchisamala pozindikira za ubwino wake.
Pamkumanuwo padali Khansala wa ward ya mtundawosema, George Jailosi yemweso wapampando wa khonsolo ya Boma la Thyolo kupezeka kwake kudali kofunika chifukwa makhansala ndi omwe amathandizira zitukuko zambiri.
Mafumu adondo monga Chimaliro, January ndi Ngolongoliwa nawoso adali pa mkumano kuimira mmidzi yawo pozindikira kuti iwowa ali ndi udindo waulukulu kumidzi komwe kumafikira zitukuko.
Apampando amakomiti owona za chitukuko kumadera (ADC), nawoso adali nawo pazokambirana za mmene chitukuko chifikere kwa anthu omwe adasankha Maureen Namwali kukhara phungu wa nyumba ya malamulo kudera la Thyolo-Goliati.